
Chipani chosutsa boma cha UDF chalengedza kuti chasankha loya Ian Nankhuni kukhala m’neneri wa chipanichi ngati mbali imodzi yokonzanso chipanichi pamene zipani zilipakalikiliki wokonzanao ntchito zake pokonzekela zisankho za mu 2030.
Kudzera mu kalata yomwe yachokera kwa Mlembi wamkulu wachipani cha UDF a Genarino Lemani, a Nankhuni asankhidwa ndi mtsogoleri wachipanichi a Atupele Muluzi.
A Lemani ati chipanichi chomwe chakhala kunja kwa boma kwa zaka 22, chayamba kutsatira ndondomeko zoika mmaudindo achinyamata komanso amai ochuluka komanso kulimbitsa komiti zake kuti chikhale cha mphamvu ndi kudzalowanso m’boma mtsogolomu.
Iye wati Chipani cha UDF akuchikonza, pamene akubweretsa achinyamata pofuna kuchipatsa moyo wina watsopano.
“A Nankhuni ali ndi kuthekera kolankhulira chipani ndipo ngati chipani tikugwira ntchito yoonetsetsa kuti UDF ikhalenso ya mphamvu ndi kudzabwereranso m’boma, mukudziwa inu kuti takhala tili kunja kwa boma kwa zaka 22,” atero a Lemani.



