

Dalitso Kabambe yemwenso ndi mtsogoleri wachipani cha UTM wapempha adindo ku boma kuti afotokozere a Malawi pa yemwe akulamulira dziko lino pamene mtsogoleri wa dziko Peter Mutharika adakali kunja kwa dziko lino.
Kudzera pa tsamba lawo la mchezo la Facebook a Kabambe ati boma libwere poyera ndikuuza a Malawi za munthu yemwe akutsogolela dziko lino pakadali pano.
Kabambe wati ulendo omwe mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika anapita ku South Africa ndi ofunika kwa iye ngati munthu koma nalo dziko likufunika mtsogoleri.
“If the President is on a private trip, that is his business. But governing the country is public business. Who is running Malawi in his absence? Malawians deserve a clear answer – not silence.” Said Kabambe.
Mutharika anachoka m’dziko muno pa 6 October 2026 kupita ku South Africa pa maulendo ake odziwika bwino kuti ‘Private Trip’ ndipo zambiri zokhudza ulendowu ndikubwelera kwake kuno ku mudzi sizikudziwika.
Chiloweleni pa mpando wa mtsogoleri wa dziko Mutharika wapita kunja kwa dziko lino ma ulendo asanu amene onse amawatchula kuti “Private Trip“
Maulendo ake onse asanu alimotere:
1st: 1 Dec 2025 – 15 Dec 2025 (Masiku 14)
2nd: 1 March 2026 – 12 March 2026 ( Masiku 11)
3rd: 12 June 2026 – 29 June 2026 (Masiku 17)
4th:5 Aug 2026 – 15 Aug 2026 ( Masiku 11)
5th: 6 Oct 2026 – Mpaka pano akuti adali ku South Africa


