
Abusa a Frank Chikapa apa Manyowe Assemblies of God odziwika ku Blantyre mdela la Manase amwalira pa ngozi ya galimoto pa malo othilira mafuta agalimoto ku Nyambadwe mu mzinda Blantyre.
Abusa a Chikapa anagundidwa ndi galimoto pamene amafuna kuthira mafuta pa filling station ya pa Nyambadwe.
Thupi la abusa a Chikapa analitengela ku nyumba ya chisoni ya Queens ndipo pali chiyembekezo choti thupili alitengera ku nyumba kwao ku Manyowe mmawa womwe uno.
Mwambo wa maliro a abusa Frank Chikapa ukachitikila ku Manyowe loweluka ndipo kenako thupi lawo alinyamulira kwao ku Machinjiri Area 7, kwa Chikapa komwe likalowe mmanda tsiku lomwelo.
Abusa a Chikapa amadziwikanso bwino ku Manyowe ngati kaswiri wodziwa kuyendesa miyambo yosiyanasiyana kapena kuti Master of Ceremony (MC) pachingelezi.



