Mkulu oyang’anira za chisankho ku chipani cha UTM a Bright Kagawa watula pansi udindo wake ku chipaniku.
Kagawa wati watula pansi udindo wakewu pazifukwa zoziwa okha.
Mneneri wachipani cha UTM a Felix Ndawala atsimikiza kuti walandira kalata ya a Kagawa yoti atula pansi udindo wawo.
Kutula pansi kwa a Kagawa kukuza patangotha masiku ochepa a Emmanuel Michael Mwanyongo omwenso amadziwika bwino kuti Yongo wa Yongo atatula pansi udindo wawo wamkulu oyang’anira ndondomeko zoyendesera chipani.
A Bright Kagawa anali nawo mugulu la mboni za UTM pa mlandu okhuza chisankho cha 2019 chomwe bwalo lamilandu linagamula kuti chichitikenso.
